Chikristu ndi Chislamu PDF Print E-mail

Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kutumikira udzaonongeka, inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu" Yesaya 60:12. Paciyam, bi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi Genesis 1:1 ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m' chifanizo chathu. Monga mwa chikhalidwe chathu: Genesis 1:26 Lero pa dziko lonse lapansi maiko ambiri adalandira ufulu odzilamurila, komankhondo imene yasautsa anthu ambiri ndi kudziwa Mulungu woona amene ayenela kumukhulupirila ndi kumulambira. Mulungu wolenga kumwamba ndi dziko lapansi anati “usakhale nayo milungu ina koma ine ndekha"

Eksodo 20:3.

 

CHISALAMU

Chislamu ndi chipembedzo chokhala ndi m'tsogoleri wake, malamulo ake ndi miyambo yakenso. M'tsogoleri wa Chislamu ndi munthu amene adamwalira dzina lake Muhammod . Muhammod anabadwa m'chaka cha 570 AD, anayamba nchito yake monga m'neneri m'chaka cha 613 AD, ndipo anamwalira mchaka cha 632 AD. Chisalamu chili ndi mizati imnene chiyadzamilapo. Olemba buku lochedwa "Understanding Islam" anati mizatiyi ilipo isanu, koma olemba "Slavery, Terrorism and Islam" Dr. Peter Hammond anati Pali mizatu isanu ndi umodzi (6) nati anthuwa anati mizati ya chipembezo chawo ndi 5, chifukwa wa 6 ndi nkhondo imene anaicha "nkhondo yoyera" Jihad.

 

Koma inayi ndi iyi:

 

1. Shahada - Kuvomereza poyera chikhulupiriro chawo.

2. Sawn - Kusala kudya mwezi wa Ramadan onse, atadya madzulo, mpaka m'wama.

3. Salah - Kupemphera kasanu pa tsiku limodzi.

4. Zakah - Kupatsa chaufulu kwa ena (koma molengeza).

  1. 5.Hajj - Ulendo wa ku Mecca ngakhale kamodzi mu umoyo onse.

Ma muslimu amakhulupirira pa zinthu 5 kuti avomerezeke kukhala m'modzi wa iwo.

 

  1. 1.Mulungu umodzi (allah).
  2. 2.Angelo alipodi.
  3. 3.Mabuku onse ovumbulutsidwa asanu olembedwa ndi Moses, Salimo la David, chipangano chatsopano ndi Quran.
  4. 4.Aneneri otumidwa ndi Mulungu pakati pawo pali Muhammod ndi Yesu.
  5. 5.Kuuka kwa a kufa, kumene kuphatikiza ulosi wa Tsiku Lomariza la chiweruzo kumene adzaonetsa kopita, m'silamu, ku Gehena kapena ku paradiso.

 

CHIKHRISTU

Chikristu ndi moyo umene umapezeka mwa m'tsogoleri amene anati ine ndine kuuka ndi moyo yense okhulupirira ine angakhale amwalira adzakhala ndi moyo" Yohane 11:25 - 26.

Zipembedzo zili ndi kumene zalinga, zili paulendo opita kumapeto, ulendo ulionse uli ndi njira yake. Mtsogoreli wa Chikristu Yesu anati: mapeto a Chikristu ndi moyo wosatha, ndipo kuti munthu akafike ku moyo wosatha, mjira yake ndi Yohane 14:6. Chikristu si chipembedzo chabe koma moyo. Akristu Buku lawo ndi Baibulo mau ake a Mulungu . Asilamu Buku lawo ndi Quran imene anati Muhammod adalandila kwa m'ngelo Gabriel.

Quran

Baibulo

Buku limodzi

Mabuku 66

Wolemba mnthu umodzi

Wolemba anthu 40

Chilankhulidwe chimodzi

Zilankhulo 3

Dziko limodzi

Makontinenti 3

Lolembedwa mu zaka23

Lombedwa mu zaka 1500

Mulibe Ulosi

Muli Ulosi

Mulibe Zodabwitsa

Muli Zodabwitsa

Manda ku Medina

Manda apululu ku Yerusalemu

Mulibe Chiwombolo

Muli Chiwombolo

Muli adani pa adani

Chikondi pa adani

Muli ukapapolo

Muli Ufulu

Pamene mukuwerenga pepala iyi, dziwani kuti mwapatsidwa mwayi osankha chimene muyenela kutsatira, chifukwa tsiku lina mwayi umenewu udzakhala utakutherani. Mudzaufuna koma sudzapezeka. Lero ngati inu mukhulupirira Ambuye Yesu mudzapulumuka. Machitidwe 16:31 pakuti palibe dzina lina limene tingapulumutsidwe nalo Machitidwe 4:12 kuti mudziwe zambiri, kapena muli ndi funso lembelani ku keyala iyi.

Print here for printable tract version of this article

 
Copyright © 2019. Frontline Fellowship. Powered by joomla
S5 Logo